
Tikamakamba za ulimi timangoyang’ana zomwe alimi akulima komanso kuweta. Tisaiwaletu kuti uchi ndi mbali imodzinso ya ulimi. Kodi zimakhala bwanji kuti uchi upezeke m’mataunimu? Kodi umaphikidwa? BOBBY KABANGO adacheza ndi mkulu wina amene akupanga ulimi wa uchiwu.
Tidziwane kaye wawa…
Ndine Happy Kaniki ndipo ndimakhala ku Chilobwe mumzinda wa Blantyre.
Chili m’botolocho n’chiyani?
Umenewu ndi uchi, mabotolo onsewa muli uchi ndithu womwe ndikugulitsa. Mukafuna mutha kupata botolo limodzi.
Ndi wabwino umenewu?
Talawani nokha, mukumva bwa? Uwutu ndi weniweni kuchokera mumn’goma.
Mumapanga bwanji uchiwu?
Sitipanga, timapeza uchi umenewu kuchoka kwa alimi pamene afula kumene. Ntchito yonse timagwira tokha mpaka kupakira m’mabotolomu.
Zimakhala bwanji kuti mulumikizane ndi alimi?
Choyamba timapeza alimi amene amafula uchi. Mwachitsanzo, pamene ndimayamba ntchitoyi, ndidalumikizana ndi alimi a ku Chintheche ku Nkhata Bay, Karonga ndi Mwanza koma ndidayambira ku Mwanza komwe ndakhala ndikupeza uchiwu.
Ndiye amakubweretserani, kapena mumapita komweko?
Ayi, mpaka akubweretsere? Timapita komweko kuti tikakhale ndi mwayi woona momwe amafulira uchi wawo komanso tikasankhe.
Zimakhala bwanji mukapitako?
Tikafikako alimiwa amabweretsa uchi wawo pamodzi ndiye mumasankha. Ndimasankha limodzi ndi iwo.
Mumachotsa ziti? Nanga mumatenga chiyani pamene mukusankha?
Timasankha zisa za madzi zokha, malesa timawasiya koma anthu ena ayamba kupempha kuti akufuna ndizibweretsa malesa. Zimenezi zichitika posachedwapa. Ndimatenga zisa za madzi chifukwa nzomwe timapezamo uchi woika m’botolomu.
Kusonyeza kuti simupita nawo kofula?
Pena timafula koma si nthawi zonse. Kwambiri ndimapeza afula kale.
Koma amadziwa kafulidwe kabwino?
Eya, adaphunzitsidwa ndi a Total Land Care, ndiye uchi wawo ngakhale mafulidwe awo zimakhala zadongosolo.
Zisazo mukatenga, mumazitani?
Amafinya alimiwo kuti atulutse uchi, apa ndiye kuti tikufunano tichotse zisa. Tikatero timatenga uchi wamadzi wokha ndi kuthira m’zigubu zomwe ndimatengeratu zokaikamo uchiwo. Apa ndiye kuti mlimi tathana naye, timawalipira n’kunyamula zigubu zathu kumabwera kuno kudzamalizitsa ntchito yokonza uchiwu.
Patsala ntchito yanji?
Timalowa gawo lachitatu. Gawo loyamba ndi kufula, gawo lachiwiri ndi kuchotsa uchi wamadzi komanso kusankha zisa. Gawo lachitatu ndi lomwe timadzachita tikabweretsa uchiwo. Apatu timayamba kusefa uchiwo.
Mumasefa chiyani?
Timasefa uchiwo, simungagwiritsire ntchito kupanda kusefa. Mukasefa lero, ndiye kuti mudikira ugone, mmawa wake timausefanso. Tikatero timaudikira kuti uziwoneka bwino. Pamene mwasefa mumapeza tina tolimba tomwe sitiyenera kulowa m’thupi mwa munthu. Ukasefedwa kachiwirika ndiye kuti watheka umenewo.
Kodi mumauphika?
Ayi, sindiphika kapenanso kuthira shuga. Uwu ndi uchi weniweni popanda zowonjezerapo. Tikuutcha kuti Multipurpose Honey.
Ndiye mumatani mukatha kusefa?
Apa ndiye kuti ntchito yopakira m’mabotolo timakhala taiyamba kuti tikasiye m’malo ogulitsira. Mabotolo ena ndimagulitsa ndekha.
Mugulitsa bwanji?
Botolo la magalamu 500 likugulitsidwa K2 000; botolo la magalamu 250 likugulidwa pa mtengo wa K1 200 pamene la magalamu 100 ndikugulitsa K500.
Ukupezeka malo ati?
Panopa ndikugulitsa ndekha, koma pofika June ukhala ukupezeka mu Shoprite, PTC ndi mashopu ena. Koma anthu akuukonda kwambiri moti ndatumizapo mabotolo ena ku Botswana, South Africa ndi Ghana.
Kodi uchiwu akutinso umathandiza kuchiza matenda ena?
Kwabasi! Matenda monga zilonda za m’mimba, mphumu, chifuwa, zilonda pakhosi, zidzolo za pakhungu ndi ena otero.
The post Kukatamuka ndi uchi wa Multipurpose appeared first on The Nation Online.