
Pamene ulimi wa thonje udayamba kalekale koma sukutukuka kwenikweni, kuwala kukhoza kuoneka kutsogoloku pamene dziko la Brazil lakonza zothandiza alimi m’dziko muno kupita patsogolo ndi thonje.
Nduna ya zamalimidwe Allan Chiyembekeza adati ntchito yotukula ulimi wa thonjeyo ithandiza kuti alimi azilima thonje lochuluka komanso lapamwamba ndipo mtengo wake uzikhala wabwino.
“Ntchitoyi itithandiza kukwanitsa masomphenya athu otukula ulimi wa thonje kuti tikwanitse zomwe msika umafuna. Ndikhulupirira kuti zimenezi zidzathandizanso kuti mitengo idzakhale yabwino,” adatero Chiyembekeza.
Ndunayi idati nthawi idafika yoti Malawi iziunguza mbewu zina zobweretsa ndalama, monga dzikoli lichitira ndi fodya, kuti chuma cha dziko chipite patsogolo.
Chiyembekeza adati ntchitoyi ithandiza kutukula malo a kafukufuku a Makoka kukhala malo aukachenjede wa zakafukufuku ndipo likulu lake lidzakhala ku Tete m’dziko la Mozambique lomwe ntchito ngati yomweyi ikuchitikanso.
“Ena amaona ngati ulimi wa thonje ulibe phindu koma boma lidakhazikitsa thonje ngati imodzi mwa mbewu zikuluzikulu zomwe dziko lino limatumiza kumaiko akunja choncho ndi mbewu yofunika kwambiri,” adatero Chiyembekeza.
Kazembe wa dziko la Brazil ku Malawi Gustavo Nogueira adati ntchitoyi ikhudza kulimbikitsa malimidwe amakono omwe akatswiri a m’dzikolo adapeza monga kuteteza kumatenda ndi tizilombo, kasamalidwe ka nthaka komanso kupititsa patsogolo ntchito za kafukufuku wa thonje.
“Ntchito yomweyi tidaigwira m’maiko ena monga Benin, Burkina Faso, Chad ndi Mali ndipo idabala zipatso zokoma kwambiri moti alimi maiko amenewo akusimba lokoma,” adatero Nogueira.
Iye adapempha alimi kuti adzadzipereke ntchitoyi ikayamba kuti phindu lake lidzaoneke.
Ntchitoyi ikhudza kuphunzitsa alangizi ndi alimi a thonje, kukhazikitsa njira zamakono zaulimi ndi kulimbikitsa zokambirana pakati pa akuluakulu oyang’anira za misika ndi alimi kuti pasamakhale kuponderezana kwa mtundu uliwonse.
Wapampando wa nthambi yoyendetsa nkhani za thonje Patrick Khembo adati ntchitoyi ikayamba ulimi wa thonje udzapita patsogolo chifukwa alimi ambiri omwe amanyozera ulimiwu adzakopeka.
Mlembi wamkulu mu unduna wa zamalimidwe, Erica Maganga, adati alimi 400 000 m’Malawi muno amadalira ulimi wa thonje ngati njira yopezera ndalama.
Iye adati boma kudzera mu undunawu lidakhazikitsa ntchito zotukula ulimi wa thonje kuti alimi a mbewuyi azipata phindu lochuluka akagulitsa kuti umphawi uchepe.
Wapampando wa bungwe la alimi a thonje, George Mnesa, adati alimi a thonje ndi odzipereka pantchito yawo koma adadandaula kuti nthawi zambiri mitengo ndiyo imabwezera mmbuyo ulimiwu.
“Alimi a thonje amalimbikira zedi koma vuto limakhalapo nthawi yogulitsa chifukwa mitengo imakhala yotsika kuyerekeza ndi zomwe alimi amalowetsa polima, mapeto ake alimi ambiri amasiya kulima,” adatero Mnesa.
Iye adati vuto lina ndi zipangizo monga mbewu yamakono, mankhwala ophera tizilombo ndi ulangizi panjira zabwino zolimira thonje.
The post Tsogolo lowala mu Thonje appeared first on The Nation Online.