Quantcast
Channel: Nation Online
Viewing all articles
Browse latest Browse all 42979

Ulipolipo pa Kamuzu Stadium lero

$
0
0
Bullets_Nomads

 

Masanawa, khwimbi la anthu likhala pikitipikiti mumsewu wa Masauko Chipembere ulendo pa Kamuzu Stadium atavala zofiira komanso za mtundu wa thambo (blue).

Kungoona makakawa, ungodziwiratu kuti ndi Mighty Be Forward Wanderers ikuphana ndi Big Bullets, masewero wonunkhira kutali ngati mvula yobzalira.Bullets_Nomads

Wanderers ikufuna iphe Bullets kuti ikhale pamwamba pa ligiyi itagonja ndi Silver Strikers sabata yatha.

Timuyi, yomwe ili pakhomo masanawa, ili ndi mapointi 21 ndipo yasewera magemu 10. Bullets ili pamwamba pa ligiyi ndi mapointi 23 ndipo yasewera magemu okwanira 11.

Kupambana wa Wanderers kuyipatsa mwayi wokwera pamwamba pa ligiyi, pamene ikapambana Bullets ndiye kuti ithawa Wanderers ndi mapointi asanu.

Kukamba za masewero a masanawa, Wanderers ndiyo ikuoneka kuti ikhala ilibe osewera monga Jimmy Zakazaka amene walowera m’dziko la Botswana kukayesa mwayi.

Timuyi isowekeranso ntchito za Muhammad Sulumba amene ali ndi makadi achikasu (red card) awiri komanso amayenera kupita ku South Africa kukayesa mwayi ndi timu ya Jomo Cosmos.

Mlembi wa Wanderers Mike Butao adauza atolankhani lachitatu kuti samulola Sulumba kupita ku South Africa komanso adalembera kalata Sulom kudandaula ndi makadi amene Sulumba alinawo ponena kuti akuganiza kuti makadiwo adabwera ndicholinga choti asasewere ndi Bullets.

“Sindife ana, zomwe zachitikazi ifeyo zikudabwitsa,” adatero Butao.

Kupatula izo, Wanderers ili mwalamwala monga akunenera mphunzitsi wawo Elijah Kananji kuti timuyi ili ndi osewera ambiri amene akhale ndi mwayi wosewera lero.

Kumbali ya Bullets, zikuonetsa kuti aliyense alipo kuphatikiza Owen Chaima amene sadasewere magemu awiri chifukwa chovulala dzanja. Naye Sankhani Mkandawire amene sadasewere masewero ndi timu ya Civo chifukwa cha makadi awiri wabwerera ku timuyi.

Mawa uliponso ku Lilongwe pamene Civo iphane ndi Silver Strikers. Awa ndi masewero ena aakulu amene ngati Silver ipambane, ndiye kuti ikwera kufika pa mapointi 22. Ngati Wanderers igonje lero, ndiye kuti Silver ili ndi mwayi wokhala pa nambala 2.

Civo ili pansi pa ligiyi ndi mapointi atatu pamene Silver ili pa nambala 3 ndi mapointi 19.

 

The post Ulipolipo pa Kamuzu Stadium lero appeared first on The Nation Online.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 42979

Trending Articles