
Bwalo la milandu m’boma la Dowa lagamula bambo wina, Limbani Jossam, wa zaka 25 kuti alipire K420 000 kapena akakhale kundende zaka zitatu popezeka wolakwa pamlandu wakuba ng’ombe zitatu.
Mneneri wapolisi ku Dowa Richard Kaponda adatsimikiza kumangidwa kwa Jossam yemwe amazengedwa mlandu ndi mnzake wina.
Woimira boma pa mlanduwu Ivy Sangwa adati Jossam ndi mnzakeyo adapita m’mudzi mwa Chibanzi T/A Msakambewa m’bomalo komwe adakaba ng’ombezo m’makola atatu.
Anthu 4 omwe adapereka umboni pa mlanduwo adanena chimodzimodzi koma wozengedwa mlanduwo amakana kuti sadabe ng’ombezo.
Sangwa adauza bwalo la milandu kuti mlandu ngati umenewu chilango chake chimalekezera zaka 14 kundende munthu akugwira ntchito ya kalavula gaga.
Jossam adamupeza wolakwa pa milandu iwiri ndipo mlandu wina adamugamula kulipira K280 000 pomwe wina adamugamula kulipira K140 000 zonse pamodzi ngati K420 000.
Iye adapempha bwalolo kuti limuganizire popereka chigamulo chifukwa amasamala ana ambiri omwe angavutike ngati iyeyo atatsekeredwa chifukwa anawo alibe munthu wina oti nkutsamirako.
“Mmanja mwangamu muli ana ambiri zedi ena ali mmasukulu ndipo onsewo amadalira ineyo pachithandizo chonse ndiye ndimati ndipemphe kuti mundiganizireko popereka chigamulo,” adatero Jossam.
Wogamula mlanduwo First Magistrate Emulani Phiri adati nzomvetsa chisoni kuti anthu ena amapalamulira dala akudziwa za udindo omwe ali nawo nkumaganiza kuti bwalo la milandu lidzawakhululukira.
Iye adati ndondomeko yoweruzira milandu ili ndi njira zake zomwe zimatsatidwa ndipo munthu aliyense amayenera kugamulidwa potsata ndondomekoyi mosayang’ana nkhope.
Sangwa amachokera m’mudzi mwa Toweza, T/A Mponela ku Dowa.
Kaponda adati mchitidwe wakuba ziweto wakula m’bomali ndipo akuchenjeza eni ziweto kuti azionetsetsa kuti ziweto zawo zili pamalo osamalika poopa kuti a tsinzina ntole angadzawayeretse m’maso.
The post Wakuba ng’ombe zitatu amulanga appeared first on The Nation Online.