Quantcast
Channel: Nation Online
Viewing all articles
Browse latest Browse all 43011

Sing’anga yonyenga ikagwira ndende zaka 12

$
0
0
arrest

Asing’anga ena si ng’anga, muchenjere nawo! Bwalo la milandu mumzinda wa Blantyre lagamula kuti sing’anga wina, amene adagonana ndi amayi awiri ndi kuwakakamiza kuti agonanenso ndi amuna awo iye akuonerera, akaseweze zaka 12 kundende.

Koma lina mwa mabanja omwe adachitidwa chipongwe ndi sing’anga Paul Luka pa 19 September chaka chatha kwa Manase mumzinda wa Blantyre, lati silidakhutitsidwe ndi chilangocho ndipo  likamang’ala kubwalo la milandu kuti mwina womangidwayu angamuonjezere zaka.

arrest“Si zoona ayi kuti munthu watigona komanso kutichititsa chikwati ndi amuna athu iye akuonerera ndiye akangokhala zaka 12 basi azikabwerako. Tipitanso kubwalo lina kuti atithandize pamenepa,” adatero mayiyo.

Mmodzi mwa amayi amene adagonedwawo adati zolaulazo zidachitika pamene adadandaulira sing’angayo kuti awathandize ndi mankhwala kuti apeze ntchito komanso kuti mwana wake achire kumatenda otupa miyendo.

Ataombeza maula ake, sing’angayo akuti adauza mayiyo kuti mwamatsenga adathiridwa madzi osambitsira maliro komanso adamubereketsa maliro kumsana, kotero akuyenera kuchotsedwa mizimu yoipayo kuti apeze mwayi wa ntchito.

Izitu akuti zidachitikira kunyumba kwa mayiyo, amene ali pabanja ndipo ali ndi ana.

“Adati ndilowe kuchipinda kwanga limodzi ndi sing’angayo komwe amati akukandichotsa mizimuyo. Apa amuna anga, mchemwali wanga ndi amuna ake, ana komanso mayi athu adakhala pabalaza kudikirira kuti andithandize,” adatero mayiyo pouza nyuzipepala ino mu September chaka chatha zitangochitika kumene.

Mayiyu adati kuchipindako, sing’angayo adamulamula kuti achotse zovala ndipo adagonana naye monga njira imodzi yochotsera mizimuyo. Izi akuti adachitiranso mchemwali wake ndipo kenaka adalamula kuti agonane ndi amuna awo iye akuonerera.

“Kuti agonane nane tidalimbana kwambiri ndiye chifukwa cha chimenecho adati abweranso mawa lake kuti adzandithandizenso ponena kuti yankho langa lichedwa ngati satero,” adatero mayiyu ndipo mmawa wake sing’angayo adabweradi.

Mayiyu adakamang’ala kupolisi pa zomwe  amayi awiriwo adachitiridwa ndipo mmene sing’angayo amabweranso kachiwiriko adadzapeza apolisi akumudikirira ndipo adangofikira m’zingwe.

Malinga ndi Roy Makumbi, wapolisi amene wakhala akuyendetsa nkhaniyi, umboni wosonyeza kuti amayiwa adagonedwa udali wovuta kupeza.

“Kuchipatala sadapeze chifukwa atawapima adapeza umuna wa amuna awo chifukwa ndiwo adagona nawo pambuyo pa kugonana ndi sing’angayo.

“Tidaitanabe mboni zina 6 ndipo apa woweruza mlandu adamupeza mkuluyu wolakwa ndi kumulamula kukakhala kundende zaka 12 pogonana ndi mayi mmodzi komanso zaka zina 12 pogonana ndi winayo koma zilango ziwirizo zoyendera limodzi,” adatero Makumbi.

Woweruza mlanduwu, Chikondi Mandala, adati ngakhale umboni wachipatala padalibe, komabe malinga ndi zomwe bwalolo lidamva, lidatsimikiza kuti sing’angayo adagonanadi ndi amayi awiriwo mowakakamiza.

Koma chigamulo cha Mandala, chomwe chidali pa 27 March, sichikukwana kwa amayiwa ndipo ati akadandaula kubwalo lina kuti pakhale chilango choposera apa.

Atafunsidwa ngati chilandirireni ‘thandizo’ la sing’angayo zinthu zasintha pamoyo wake, iye adati mavuto adakalipo.

“Mpaka lero, achimwene, sindidalembedwebe ntchito. Ndili ndi laisensi yoyendetsera galimoto koma ntchito sindikuipeza,” adatero iye.

Nanga kumbali ya matenda a mwana wake?

“Matendawo ndiye adasiya koma si kuti adasiya chifukwa cha thandizo la sing’angayo. Ndidapita naye kuchipatala komwe adandipatsa thandizo,” adatero.

Sing’anga Luka pano ikusungidwa kundende ya Chichiri. Iye ngwa m’mudzi mwa Mbinda kwa Senior Chief Somba m’boma la Blantyre.

 

The post Sing’anga yonyenga ikagwira ndende zaka 12 appeared first on The Nation Online.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 43011

Trending Articles