Quantcast
Channel: Nation Online
Viewing all articles
Browse latest Browse all 42998

Kusanthula mitundu ya adzukulu pamaliro

$
0
0

Nthawi zambiri pazovuta anthu akamva dzina lakuti adzukulu amaganiza za anyamata okumba manda, komatu akuti liwuli ndi ulemu womwe umaperekedwa kwa anthu omwe amapatsidwa maudindo osiyanasiyana pamaliropo. STEVEN PEMBAMOYO adacheza ndi T/A Nthondo ku Ntchisi yemwe akutambasula za mitundu ya adzukulu, ntchito zawo, milandu yomwe amapalamula ndi zilango zake.

 

Kodi akati adzukulu pazovuta amatanthauzanji?

Liwuli limatchulidwa pofuna kulemekeza munthu kapena anthu omwe apatsidwa mbali yochita pazovuta. Mwachidule pali mitundu ingapo ya adzukulu koma mwina titakambapo za mitundu inayi kaye. Pali adzukulu a kumanda, adzukulu a kumoto, adzukulu a kusiwa ndi adzukulu a bwalo.

 

Adzukulu akumanda ndi ati?

Amenewa ndi gulu la anyamata omwe amakakumba dzenje loikamo womwalirayo. Amakhala anyamata chifukwa ntchito yomwe imakhala kumeneko ndi yoyenera amuna. Kwambiri ntchitoyi imakhudza kukumba ndi kufukula dothi zomwe amayi si kwenikweni.

 

Ndimamva kuti adzukulu a kumanda akatha ntchito yawo amayenera asukusule kumanda komweko. N’chifukwa ninji amakakamizidwa kutero?

Timaopa kuti ena akhoza kutenga dothi la padzenje lomwe limakumbidwalo lokhalira m’mapazi kapena m’zovala nkukagulitsa kwa opanga zizimba kapena iwo amene kukachitira mankhwala chifukwa dothi limene lija ndi loipa kwambiri.

 

Nanga bwanji maliro akakhala a mwana wongopitirira amayi amakakumba okha?

Maliro amene aja amati nsenye, kutanthauza kuti ndi a mwana yemwe sadafike pa umunthu ayi. Amasiyana ndi mwana woti wabadwa, anthu amuona n’kumwalira. Amene uja ndi munthu wokwana. Tsono chimene amayi amakakumbira okha manda n’chakuti munthu wamwamuna akaponda pamanda a nsenye miyendo imatupa ndipo amangoonda mpaka kufa.

 

Nanga adzukulu a kumoto?

Amenewa ndi gulu la atsikana kapena azimayi omwe akadaberekabe pamudzi. Ntchito yawo ndi ya chizimayi monga kuphikira anthu a pasiwa, kutunga madzi ogwiritsa ntchito pasiwa ndi ntchito zina za kumoto kapena kuti kukhitchini.

 

Nanga adzukulu a musiwa?

Awa amakhala azimayi akuluakulu omwe adasiya kubereka. Iwo amangokhala m’nyumba yomwe muli maliro chozungulira pomwe mtembo wagona ndipo amachitiridwa chilichonse.

 

N’chifukwa chiyani amakhala azimayi osiya kubereka?

Mbali imodzi umakhala ngati ulemu wawo chifukwa amakhala kuti agwira ntchito nthawi yaitali. Amakhala kuti panthawi yomwe amabereka adagwirapo ntchito za adzukulu a kumoto tsono uku n’kupuma chabe. Nthawi zina ndi amayi amenewa omwe amakhala akutonthoza anamalira musiwamo ndi kumanda.

 

Tsopano adzukulu a bwalo ndiye ati?

Awa ndi adzukulu omwe amakhala akugwira ntchito zina ndi zina za pamaliropo monga kukhoma bokosi ndi kutumikira monga kumbali yomwaza mauthenga. Amenewa ntchito yawo imathera kumudzi, simafika kumanda.

 

Nanga milandu yokhudzana ndi adzukulu imakhala yotani?

Pali mitundumiyundu ya milandu. Ndiyambe ndi kumoto. Mdzukulu wa kumoto amatha kumuimba mlandu wa ulesi ngati salimbikira nawo pogwira ntchito, mwina amakonda kubwera mochedwa anzake ali pafupi kumaliza ntchito, koma amatengera kuti chakhala chizolowezi; osangoti wachedwa kamodzi ayi. Penanso amatha kumuimba mlandu wosayenda m’maliro popanda chifukwa chomveka bwino. Musiwa mokha ndiye simukhala milandu yodetsa nkhawa.

 

Nanga kumanda ndi pabwalo?

Pabwalo mlandu waukulu ndi kuchita mwano atatumidwa kapena kubwera ataledzera n’kumasokoneza, pomwe kumanda ndiye kumakhala zifukwa zikuluzikulu. Kungofika mochedwa kokumba manda umakhala mlandu ndipo umalipira; kukana ntchito kumandako ndi mlandu wina; kuledzera n’kumasokoneza zinthu ndi mlandunso.

 

Zilango za milanduyi ndi zotani?

Milandu yonseyi eni ake akakambirana zomwe agwirizanazo amakafotokozera mandoda a pamudzi. Chilango choyamba chimakhala kulipira ndipo ngati wolakwayo wakana kapena walephera kulipirako amachotsedwa mugulu la anzake kaya n’kumoto, kumanda kapena pabwalo.

 

Zikatero?

Zikatero ndiye kuti munthu woteroyo wadzipatutsa yekha pamudzi, kutanthauza kuti china chilichonse chomwe chingamuonekere akuyenera kuthana nacho yekha, kaya ndi matenda kapena maliro amene.

Zikafika apa ndi zija amati amfumu akana kulengeza maliro m’mudzi mwawo. Chimakhala chilango mpaka namfedwayo atalipira ndipo dipo lake limakhala lalikulu kusiyana ndi lomwe adakana kulipira nthawiyo.n

The post Kusanthula mitundu ya adzukulu pamaliro appeared first on The Nation Online.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 42998

Trending Articles