
Pamene munthu ali ndi chisoni amakhoza kuchita zinthu zoipa monga kudzipha pofuna kulekana nawo mavuto.
Pakadalipano nkhani imene ikusowetsa tulo ndi ya anthu amene adakhudzidwa ndi madzi osefukira m’madera osiyanasiyana m’dziko muno amene akukhala moyo wopanda chiyembekezo.
Ambiri mwa anthuwa chithandizo cha zakudya, zofunda ndi zina zambiri alandira koma funso n’kumati kodi akumakhala ndi nthawi ya phwete?
Bungwe la Malawi Red Cross Society (MRCS) ku Zomba ndi limodzi mwa mabungwe m’bomali, koma ilo ladza ndi kalumo kakuthwa pogwira ntchito ndi Akafula kufalitsa uthenga wawo.
Bungweli lili pakalikiriki kuphunzitsa komanso kulimbikitsa anthu okhudzidwa ndi madziwa kuti azikhala moyo waukhondo poopetsa kuti angaonjezere mavuto potenga matenda m’misasa kaamba ka uve.
Monga ndiwo zimazuna ndi mchere, chimodzimodzi uthenga wa zaukhondowu ukuyaza m’mitima ya anthu chifukwa cha kupezeka kwa Akafula kumisonkhano ya zaumoyoyi.
Clement Banda, mmodzi wa Akafula m’bomali, adati iye luso lake lalikulu ndi losewera nthabwala, kuvina komanso kuimba.
Pamsonkhano wina wa zaukhondo Clement atalowa m’bwalo anthu ambiri ankakayika kuti apangamo zakupsa. Koma pofuna kutsutsa khamulo kuti phwiti sachepa ndi mazira ake, mkuluyutu adayamba kuvumbulutsa nthabwala zake amvekere: “Ndipemphe atsikana nonse a dera lino kuti mundilembere ma ‘application’ ndipo amene nditamuchite ‘shortlist’ ndidzamuitana ku ‘interview’,” adatero Clement, kusiya anthu akufa nalo phwete.
Kenako adapitiriza: “Chonde, chonde makolo limbikitsani atsikana anu kuti asachite chidodo kulemba kalatazo chifukwa ndikufuna ndisiye timbewu ting’onoting’ono kuno timene sitingakokoloke ndi madzi.” Apa anthu adagwa nayo nseko.
Atatsiriza nthabwalazi Clement adamuuza osewera nyimbo (DJ) kuti amuikire nyimbo yovinika bwino.
Nyimboyi itaponyedwa, Clement adavina modolola, akupukusa chiuno chake mwaluso, zinthu zimene zidachititsa anthu owonererawo kufuula ndi chimwemwe.
Nyimbo itatha, anthu akusekabe, Clement adati: “Tamvetserani, inetu kuvina konseku n’chifukwa choti ndili ndi thanzi. Ndikanakhala kuti ndikudwala kolera, mphere ndi matenda ena amene amadza chifukwa cha uve si bwenzi ndili pano, mwina ndikadakhala nditagonekedwa kuchipatala kapena ndikugona kunyumba.
“Kotero, pamene mukukhala mumisasa, chonde yetsetsani kumakhala moyo waukhondo ndi cholinga chakuti musatenge matenda ena alionse,” adatsiriza chotero Clement.
Adamaliza uthenga wake motere: “Kufupika msinkhu si kuti nzeru zanga ndi zofupikanso. Ndimayetsetsa kuganiza mwakuya kuti ndizidzipezera zofuna za moyo wanga, osati kumangopemp-hapempha chifukwa zinthu zopemphetsa kutukwanitsa,” adatero Clement.
The post Akafula asangulutsa osungulumwa appeared first on The Nation Online.